Judges 13:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mngelo wa Chauta adauza Manowa kuti, “Ngakhaletu mukundidikiritsa chakudyacho, ine sindidya ai. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza, muipereke kwa Chauta.” (Monsemo nkuti Manowa ali wosazindikira kuti mlendoyo ndi mngelo wa Chauta.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.