Judges 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Manowa adatenga kamwanakambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya, nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Chauta, Iye amene amachita zodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Manowa anatenga mwana wa mbuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anacita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyereo