Judges 13:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene malaŵi a moto ankakwera kumwamba kuchokera paguwapo, mngelo wa Chauta uja adakwera m'malaŵi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuyang'ana. Apo iwo adadzigwetsa pansi, naŵeramitsa mitu pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kunali, pakukwera lawi la mota pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.