Judges 13:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mkazi wake adati, “Akadakhala kuti Chauta akufuna kutipha, sakadailandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu cha chakudya chija. Ndiponso sakadatiwonetsa zinthu zonsezi kapenanso kutiwuza tsopano zinthu zonga ngati zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mkazi wace ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino.