Judges 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wa Chauta adamuwonekera mkaziyo namuuza kuti, “Inu mai, ngakhale mpaka pano muli opanda ana, komabe mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.