Judges 13:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ndithu mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa, kumutu kwake kusadzapite lumo, pakuti mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulikira Mulungu kuyambira tsiku la kubadwa kwake. Ndipo adzayambapo ntchito yopulumutsa Aisraele kwa Afilisti.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.