Judges 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkaziyo adadzauza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kuno, ndipo nkhope yake inali yoopsa kwambiri ngati nkhope ya mngelo wa Mulungu. Sindidamufunse kumene akuchokera, iyenso sadandiwuze dzina lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;