Judges 13:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chosaloledwa chilichonse, chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, wopatulikira Mulungu, kuyambira tsiku la kubadwa kwake mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye ciri conse codetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire mpaka tsiku la kufa kwace.