Judges 13:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adamvera pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu uja adabweranso kwa mkaziyo nampeza atakhala pansi m'munda. Koma mwamuna wake Manowa sanali nao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwamuna wake Manowa palibe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwanuna wace Manowa palibe.