Judges 14:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samisoni adaŵauza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi! Mukandiwuza tanthauzo lake, asanapite masiku asanu ndi aŵiri a phwando, ndidzakupatsani zovala zabafuta makumi atatu ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;