Judges 14:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lachinai lake iwo adauza mkazi wa Samisoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako, kuti atiwuze tanthauzo lake la mwambi uja, mwinamwina tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya bambo wako. Monga inu mwatiitana kuno kuti mutisandutse osauka?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anati kwa mkazi wa Samsoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi mota. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?