Judges 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mkazi wa Samisoni adayamba kulira pamaso pa mwamuna wake namuuza kuti, “Inu mumadana nane, simundikonda konse. Mwaŵaphera mwambi anthu a m'dziko mwangaŵa, koma ine osandiwuzako tanthauzo lake.” Apo Samisoni adamuuza kuti, “Ona, ngakhale bambo wanga ndi mai wanga sindidaŵauze, ndiye ndingauze iweyo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi wa Samisoni analira pamaso pake, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.” Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi wa Samsoni analira pamaso pace, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?