Judges 14:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkaziyo ankangomulirira masiku onse asanu ndi aŵiri aphwandowo. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adamuuza, chifukwa chakuti adaamkakamiza kwambiri. Pompo mkaziyo adakauza anthu a m'dziko mwake aja tanthauzo la mwambiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analira pamaso pace masiku asanu ndi awiriwo pocitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lacisanu ndi ciwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wace mwambiwo.