Judges 14:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu amumzinda aja adauza Samisoni pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri dzuŵa lisanaloŵe, kuti, “Nchiyani chozuna kuposa uchi? Nchiyani champhamvu kuposa mkango?” Samisoni adaŵauza kuti, “Mukadapanda kulima ndi msotiwang'ombe wanga, simukadatha kumasula mwambi wangawu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa, Chozuna choposa uchi nchiyani; ndi champhamvu choposa mkango nchiyani? Pamenepo ananena nao, Mukadapanda kulima ndi ng'ombe yanga, simukadatha kumasulira mwambi wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti, “Chozuna nʼchiyani choposa uchi? Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?” Samsoni anawawuza kuti, “Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono, simukanatha kumasulira mwambi wangawu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samsoni tsiku lacisanu ndi ciwiri, lisanalowe dzuwa, Cozuna coposa uci nciani; ndi camphamvu coposa mkango nciani? Pamenepo ananena nao, Mukadapanda kulima ndimthandi wanga, Simukadakumika mwambi wanga.