Judges 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni mwamphamvu ndipo Samisoniyo adapita ku Asikeloni nakapha anthu makumi atatu am'mudzimo ndipo adatenga zovala zao za tsiku lachikondwerero, nazipereka kwa amene adamasula mwambi aja. Ndipo adabwerera ku nyumba ya bambo wake ali wokwiya kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samsoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zobvala zao, nawapatsa okumika mwambiwo zobvala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kumka ku nyumba ya atate wace.