Judges 14:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma bambo ndi mai wake adamufunsa kuti, “Kodi palibe mkazi woti ungakwatire pakati pa ana a achibale akoŵa kapena pakati pa anthu a mtundu wathu, kuti uzikatenga mkazi pakati pa Afilisti, anthu osaumbalidwa?” Koma Samisoni adauza bambo wake kuti, “Ine ndiye kanditengereni yemweyo, pakuti ndiye ndamkonda kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?” Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atate wace ndi amai wace ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samsoni kwa atate wace, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.