Judges 14:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo ndi mai wake sankadziŵa kuti zimenezo zinali zochokera kwa Chauta, pakuti Chauta ankafunafuna poŵapezera chifukwa Afilistiwo. Nthaŵi imeneyo nkuti Afilisti akulamulira Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atate wace ndi amai wace sanadziwa kuti cidacokera kwa Yehova ici; popeza analikufuna kutola cifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israyeli.