Judges 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Samisoni adapita ku Timna pamodzi ndi bambo ndi mai wake. Atafika ku minda yamphesa ya ku Timna, Samisoni adamva mwanawamkango akumdzumira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatsikira Samisoni, ndi atate wake ndi mai wake ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anatsikira Samsoni, ndi atate wace ndi mai wace ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.