Judges 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni ndi kumsandutsa wankhongono. Motero ngakhale analibe chida m'manja, Samisoni adakadzula mkangowo, monga momwe munthu amakadzulira kamwanakambuzi. Koma sadauze bambo kapena mai wake zimene adachitazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwana wa mbuzi, wopandakanthu m'dzanjaliace; koma sanauza atate wace kapena amai wace cimene adacicita.