Judges 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samisoni adafula njuchizo, natenga uchi m'manja ndi kumapita naadya. Atafika kwa bambo ndi mai wake, adaŵapatsako uchiwo, iwo naadya. Koma sadaŵauze kuti uchiwo adaufula mu mkango wakufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaufula ndi dzanja lake, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wake ndi amai wake, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauze kuti adaufula uchiwo m'chitanda cha mkango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.