Judges 15:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita kanthaŵi, pa nyengo yodula tirigu, Samisoni adapita kukacheza kwa mkazi wake, atatenga mwanawambuzi. Ndipo adati, “Ndikufuna kukaloŵa m'chipinda cha mkazi wanga.” Koma bambo wake wa mkaziyo adamkaniza kuloŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kuceka tirigu Samsoni anakaceza ndi mkazi wace ndi kumtengera mbuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kucipinda. Koma atate wace sanamlola kulowamo.