Judges 15:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Yuda adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwadzamenyana nafe?” Iwowo adayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samisoni kuti timchite zomwe iye adatichita ife.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?” Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera cifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samsoni, kumcitira iye monga anaticitira ife.