Judges 15:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu 3,000 a ku Yuda adapita ku phanga la ku Etamu, namufunsa Samisoni kuti, “Kodi sukudziŵa kuti Afilisti ndiwo amene amatilamulira? Nanga izi watichitazi nzotani?” Iye adaŵayankha kuti, “Ndaŵachita zomwe iwowo adandichita ine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?” Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu, nati kwa Samsoni, Sudziwa kodi kuti Atilisti ndiwo akutilamulira ife? nciani ici waticitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandicitira ine ndawacitira iwo.