Judges 15:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwowo adamuuza kuti, “Tabwera kudzakumanga kuti tikakupereke kwa Afilisti.” Samisoni adaŵauza kuti, “Lonjezeni molumbira kuti simundipha ndi inuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Afilisti, Nanena nao Samisoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.” Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Atilisti. Nanena nao Samsoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.