Judges 15:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adamuuza kuti, “Iyai. Ife tingokumanga chabe nkukakupereka kwa iwowo. Sitikupha ai.” Choncho adammanga ndi zingwe ziŵiri zatsopano, namtulutsa m'phanga muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kuchokera kuthanthwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kucokera kuthanthwe.