Judges 15:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samisoni atafika ku Lehi, Afilisti adabwera akufuula kudzamchingamira. Pompo Mzimu wa Chauta udamtsikira mwamphamvu, ndipo zingwe zimene adammanga nazo zija zidasanduka ngati thonje logwira moto, zidachita ngati kusungunuka nkuchoka m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika ku Leki Afilisti anapfuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ace zinanga bwazi lopserera ndi moto, ndi zomangira zace zinanyotsoka pa manja ace.