Judges 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Samisoni adayamba kuimba nyimbo yakuti, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu! Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu chikwi chimodzi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Samisoni, Ndi chibwano cha bulu, miulumiulu, amuna chikwi ndawakantha ndi chibwano cha bulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Samsoni anati, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu. Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu 1,000.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Samsoni, Ndi cibwano ca buru, miuru miuru, Amuna cikwi ndawakantha ndi cibwano ca buru.