Judges 15:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Samisoni adamva ludzu kwambiri ndipo adatana Chauta mopemba nati, “Inu mwapereka chipulumutso chachikulu choterechi kudzera mwa ine mtumiki wanu. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osaumbalidwaŵa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu cipulumutso ici cacikuru ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?