Judges 15:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bamboyo adamuuza kuti, “Ine ndidaatsimikiza kuti mukudana naye kwambiri mkaziyu. Choncho ndidamkwatitsa kwa mnzanu uja. Kodi mng'ono wake si wokongola kupambana iyeyu? Pepani ndithu, ingotengani ameneyu m'malo mwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng'ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m'malo mwa winayu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati atate wace, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi tako; mng'ono wace sakoma koposa iye nanga? ukhale naye, m'malo mwa winayu.