Judges 15:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atayatsa nsakalizo, adazitaya nkhandwezo kuti zipite m'minda yatirigu ya Afilisti. Popitapo zidakatentha milu ya tirigu ndi tirigu wosadula yemwe, pamodzi ndi mitengo ya olivi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosaceka wa Afilisti, natentha miulu ndi tirigu wosaceka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.