Judges 15:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Afilisti adayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita zimenezi?” Ena adayankha kuti, “Ndi Samisoni, mkamwini wa Mtimuna uja, amene wachita zimenezi, chifukwa chakuti Mtimunayo watenga mkazi wa Samisoni kumkwatitsa kwa mnzake.” Tsono Afilisti adabwera namtentha mkaziyo pamodzi ndi bambo wake yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.” Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Afilisti anati, Wacita ici ndani? Nati, Samsoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wace, nampereka kwa mnzace. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wace ndi moto.