Judges 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Delila adatenga zingwe zatsopano nammanga nazo, nafuula kwa iye kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Monsemo nkuti anthu amene ankambisalira aja ali m'chipinda cham'kati. Koma, Samisoni adangomwetula zingwezo kumanja kwake ngati thonje.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Ndi omlalira analikulinda m'chipinda cha m'kati. Koma anazidula pa manja ake ngati thonje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Delila anatenga zingwe zatsopano namumanga nazo. Kenaka anati “Amuna anga, Afilisti aja afikanso!” Nthawi iyi nʼkuti anthu omubisalira aja ali mʼchipinda chamʼkati. Koma iye anadulanso zingwe mʼmanja ake ngati akudula ulusi wa thonje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Atilisti akugwera, Samsoni. Ndi omlalira analikulinda m'cipinda ca m'kati. Koma anazidula pa manja ace ngati thonje.