Judges 16:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Delila adauzanso Samisoni kuti, “Mpaka tsopano lino mwakhala mukundipusitsa ndi kumandinamiza. Tandiwuzani m'mene munthu angathe kukumangirani.” Samisoni adamuuza kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwanga uzilukirira m'cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi anthu ena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze chimene angakumange nacho. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Delila anati kwa Samsoni, “Mpaka tsopano mwakhala mukundipusitsa ndi kumandiwuza zabodza. Chonde, tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.” Iye anayankha kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziwiri za kumutu kwanga utazilukira mu cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala wofanana ndi munthu wina aliyense.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze cimene angakumange naco. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.