Judges 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho pamene Samisoni ankagona, Delila adatenga njombi za kumutu kwa Samisoni nazilukirira m'cholukira nsalu. Ndipo adachimanga molimbika ndi chikhomo nafuula kwa Samisoni kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adadzukira kutulo nazula chikhomocho, ndipo njombi zake zidachoka m'cholukira chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samisoni; nagalamuka iye patulo take, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iye akugona, Delila analukira njombi za ku mutu kwa Samsoni mu cholukira nsalu nachimanga molimba ndi chikhomo. Pambuyo pake anati kwa Samsoni, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Tsono iye anadzuka ku tulo, nazula chikhomo chija ndipo njombi zinachoka mu cholukira chija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samsoni; nagalamuka iye patulo tace, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.