Judges 16:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mkaziyo adamufunsa kuti, “Mungathe bwanji kunena kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Mwakhala mukundipusitsa katatu konseka, ndipo simudandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? Wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo muchokera mphamvu yako yaikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mkaziyo ananenanso kwa iye kuti, “Munganene bwanji kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Aka ndi kachitatu mukundipusitsa ndipo simunandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo mucokera mphamvu yako yaikuru,