Judges 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adamuululira mkaziyo maganizo ake onse namuuza kuti, “Pamutu pangapa sipanapite lumo, popeza kuti ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu, kuyambira ndili m'mimba mwa mai wanga. Atangondimeta tsitsi langali, mphamvu zanga zidzandichokera. Ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anamuwuza mkaziyo zonse za mu mtima mwake nati “Lumo silinapitepo pa mutu wanga chifukwa ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu chibadwire. Ngati nditametedwa mphamvu zanga zidzandichokera, ndidzasanduka wofowoka ndipo ndidzafanana ndi munthu wina aliyense.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo anamfotokozera mtima wace wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu ciyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandicokera, ndidzakhala wofoka wakunga munthu wina ali yense.