Judges 16:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Delila adaona kuti waulula maganizo ake onse, adatuma uthenga kukaŵaitana akalonga a Afilisti aja ndipo adaŵauza kuti, “Bweraninso kamodzi kokha, pakuti wandiwululira maganizo ake onse.” Tsono akalonga a Afilisti adafika kwa mkazi uja atatenga ndalama m'manja mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wake wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wake wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wace wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wace wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao.