Judges 16:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Gaza adauzidwa kuti, “Samisonitu adabwera kuno.” Tsono anthuwo adazinga malowo namubisalira usiku wonse pa chipata cha mzinda. Iwo adakhala chete usiku wonsewo namanena kuti, “Tiyeni tidikire mpaka m'maŵa kutacha, pamenepo timuphe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mudzi, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wina anauza a ku Gala, ndi kuti, Samsoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa cipata ca mudzi, nakhala cete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kuca, pamenepo tidzamupha,