Judges 16:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Delila adafuula kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Samisoni adadzuka akuganiza kuti, “Ndituluka monga momwe ndimachitira nthaŵi zonse, ndipo ndidzimasula.” Koma sadadziŵe kuti Chauta wamsiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake mkaziyo anamuyitana kuti, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Iye anadzuka kutuloko, naganiza kuti, “Ndituluka monga ndimachitira nthawi zonse ndi kudzimasula.” Koma sanadziwe kuti Yehova wamuchokera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samsoni. Nagalamuka iye m'tulo tace, nati, Ndizituruka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwa kuti Yehova adamcokera.