Judges 16:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina akalonga a Afilisti adasonkhana kudzapereka nsembe yaikulu kwa Dagoni mulungu wao ndi kudzakondwerera, pakuti ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa Samisoni, mdani wathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m'dzanja lathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono atsogoleri a Afilisti anasonkhana kuti adzapereke nsembe yayikulu kwa Dagoni mulungu wawo ndi kukondwerera popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu mʼmanja mwathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikuru, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu m'dzanja lathu.