Judges 16:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu adamuwona, adayamba kutamanda mulungu wao. Ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa mdani wathu, munthu woononga dziko lathu uja amene adapha anthu ambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo atamuona Samsoni, anayamba kutamanda mulungu wawo popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka mdani wathu mʼmanja mwathu, ndiye amene anawononga dziko lathu, napha anthu athu ambirimbiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.