Judges 16:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mitima yao inkasangalala adati, “Muitaneni Samisoni kuti adzatisangalatse.” Choncho adamtulutsa m'ndende, ndipo iye adayamba kuŵasangalatsa. Kenaka adamuimiritsa pakati pa mizati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali mʼkati mosangalala, anthu aja amafuwula kuti, “Mutulutseni Samsoniyo kuti adzatisangalatse.” Choncho anamutulutsadi Samsoni mʼndende, ndipo anawasangalatsadi. Ndipo anamuyimiritsa pakati pa mizati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samsoni, atisewerere. Naitana Samsoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuika iye pakati pa mizati.