Judges 16:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'menemo nkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu, amuna ndi akazi. Akalonga onse a Afilisti anali momwemo, ndipo padenga pake panali pafupi anthu 3,000, amuna ndi akazi, amene ankaonera Samisoni akuseŵera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samsoni.