Judges 16:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Samisoni adatama Chauta mopemba nati, “Inu Chauta, kumbukireni kamodzi kokhaka, ndapota nanu, ndipo mundilimbitse Inu Mulungu, kuti ndiŵalipsire Afilistiŵa chifukwa cha maso anga aŵiriŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Samsoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, dikupempha mundikumbukile, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, cifukwa ca maso anga awiri.