Judges 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Samisoni adagona mpaka pakati pa usiku. Pakati pa usikupo adadzuka, nagwira zitseko zapachipata ndi mafuremu ake onse aŵiri. Adazizula pamodzi ndi mpiringidzo ndi zina zonse. Adazisenza pa phewa, napita nazo pamwamba pa phiri loyang'anana ndi Hebroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba pa phiri lili pandunji pa Hebroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Samsoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa cipata ca mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazicotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ace, nakwera nazo pamwamba pa phiri liri pandunji pa Hebroni.