Judges 16:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Samisoni adati, “Ndifere kumodzi ndi Afilistiŵa.” Tsono adakankha ndi mphamvu zake zonse, ndipo nyumbayo idaŵagwera akalonga aja pamodzi ndi anthu onse aja amene anali m'menemo. Choncho kuchuluka kwa anthu amene Samisoni adaŵapha pa nthaŵi ya kufa kwake kudaposa kwa anthu amene iye adaŵapha pa nthaŵi imene anali moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Samsoni anati, “Ndife nawo pamodzi!” Nthawi yomweyo anakankha ndi mphamvu zake zonse ndipo mizati inagwera atsogoleri a Afilisti ndi anthu onse anali mʼmenemo. Tsono chiwerengero cha anthu amene Samsoni anapha pa nthawi ya imfa yake chinaposa cha iwo amene anawapha akanali ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Samsoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwace anaposa amene anawapha akali moyo.