Judges 16:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akalonga a Afilisti adabwera kwa mkaziyo namuuza kuti, “Umnyengerere mwamunayu, uwone pamene pagona mphamvu zake zoopsazi ndiponso m'mene tingathe kumpambanira, kuti timmange ndi kumgonjetsa. Ukatero, aliyense mwa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akalonga a Atilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo mucokera mphamvu yace yaikuru, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa ali yense ndalama mazana khumi ndi limodzi.