Judges 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo ataika anthu ombisalirawo m'chipinda cham'kati. Kenaka adafuula kwa mwamuna wake kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adangomwetula nsingazo monga m'mene imamwetukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zakezo sichidadziŵikebe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anali nao omlalira m'cipinda ca m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samsoni, Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka nkhosi ya bwazi pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yace siinadziwike.