Judges 17:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mika adamuuza kuti, “Khalani ndi ine, mukhale mlangizi wanga ndi wansembe wanga, ine ndizikupatsani ndalama zasiliva khumi pa chaka, ndizikupatsaninso zovala ndi zakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndarama khumi pacaka, ndi cobvala cofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.