Judges 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyu adauza mai wake kuti, “Pamene munthu adaakuberani ndalama zasiliva 1,100, inu mudaamutemberera wakubayo, matembererowo ine ndidaŵamva. Ndalamazo ndi izi, zili ndi ine. Ndine ndidaatenga.” Mai wakeyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitse mwana wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.” Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati kwa amai wace, Ndarama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndaramazo ndiri nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wace anati, Yehova adalitse mwana wanga.